National

Tiyeni tisamale chilengedwe m’mizinda yathu-CURE

By Chisomo Phiri

Limodzi mwamabungwe odziwika bwino pankhani zoteteza zachilengedwe mdziko muno la Coordination Union for the Rehabilitation of the Environment ( CURE) lapempha anthu okhala  m’mizinda yadziko lino kuti ateteze komaso kusamalira malo omwe akusunga zinthu zachilengedwe monga mitengo ndi zina zambiri m’mizindayi.

Bungweli lanena izi loweluka pomwe ilo ndi mabungwe ena amadzala mitengo pafupipafupi 1000 pamalo otchedwa Njamba Freedom Park munzida wa Blantyre.

Malinga ndi wapampando wabungweli a Maynard Nyirenda, malo monga Njamba Freedom Park komanso Michiru Mountain Nature sanctuary munzida wa Blantyre ndi ena mwa malo omwe amachititsa kuti mzinda wa Blantyre uzioneka bwino choncho ayenera kusamalidwa ndikutetezedwa bwino.

A Nyirenda anati mzovetsa chisoni kuti pali anthu omwe akuononga malo ngati awa kudzera mukuotcha makala ndi zina zotelo.

“Njamba Freedom Park ndi malo omwe ayenera asamalidwe bwino. Tiyeni tiyikepo mtima kusamalira chilengedwe kuti mizinda yathu izioneka bwino,” anatero a Nyirenda.

Iwo anaonjezera kutsutsana ndi ganizo laboma la boma la Democratic Progressive Party (DPP) lomwe limafuna kumanga malo azamasewero pa Njamba Freedom Park ponena kuti izi zitha kuononga zachilengedwe zomwe zili pamalowa.

M’mawu ake, mfumu ya mzinda wa Blantyre a Wild Ndipo omwe anali mlendo olemekezeka pa mwambo odzala mitengowu, anati iwo ndi okonzeka kupititsa chitsogolo nkhani zoteteza chilengedwe mumzindawu.

“Ife ndife okonzeka kukhwimitsa chitetezo ku zachilengedwe ndipo sitidzalora kuti malo omwe akusunga zachilengedwe mumzinda wathu uno awinongedwe,” anatero a Ndipo.

Iwo anayamikira bungwe la CURE ndi mabungwe ena onse omwe anatenganawo gawo pa mwambo odzala mitengo mumzindawu komaso kuphunzitsa anthu amumzindawu za ubwin osamala zachilengedwe.

Tags

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Close