Entertainment

Oyimba Katelele Ching’oma wamwalira

By Chisomo Phiri

M’modzi mwa oyimba odziwika bwino mdziko muno Katelele Ching’oma wamwalira.

Malinga ndi mchimwene wake wa oyimbayu, Elvis Ching’oma, oyimbayu wamwalira m’bandakucha wa lero ku chipatala cha Kamuzu Central ku Lilongwe atadwala nthenda yokhudza chiwindi.

Elvis yemwenso amajambula nyimbo za Katelele wati oyimbayu anamutumiza kuti akalandire thandizo ku chipatalachi kuchokera ku Dedza komwe amakhala.Iye wati banja la Ching’oma lisowa ntchito za oyimbayu ponena kuti anachititsa kuti banja la Ching’oma lidziwike kamba ka nyimbo zake zomwe a Malawi ambiri amazikonda.

Katelele adadziwika kwambiri mchaka Cha 2009 ndi nyimbo zake monga, Asowe, Ndili nawo mwayi ndi zina zambiri.

Tags

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Close