National

Nduna ya za mtengatenga a Jacob Hara idandaula kamba ka kuchedwa kwa ntchito ya nseu wa magawo asanu ndi limodzi (Six Lane)

By Linda Kwanjana

Nduna yoona ntchito za mtengatenga ndi mtokoma a Jacob Hara apempha kampani ya ku China yomwe ikumanga mseu wa magawo asanu ndi limodzi (6 lane) omwe ukuchokera pa kunyumba ya malamulo ndipo ukupita ku Shoprite kuti achilimike pogwira ntchito iyi.

Polankhula pomwe anayendera ntchito imeneyi, a Hara anati ndi zodandaulitsa kuti ntchito iyi yachedwa ndipo ikutsutsana ndi masomphenya a mtsogoleri wa dziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera omwe akuti akufuna ntchito izi zithe mwachangu muthawi yake yomwe inalonjezedwa.

Hon Hara-ndi ena omwe akugwila ntchito yomanga misewu

A Hara anati ntchito zomanga mseu uwu ndi zofunika kwambiri choncho zikuyenera kufulumira.

Iwo anati amvetsedwa kuti kuvuta kwa mafuta ndi komwe kwachedwetsa ntchito iyi koma iwo anati komabe anthuwa afulumire ndipo awapatsa pa 24 July 2024 kuti ndilo tsiku lomaliza loti amalize ntchito iyi.

Naye phungu wa dela limeneli a Alfred Jiya anati ntchito iyi ikatha ithandiza kwmabiri anthu okhala mdela lake. Iye anati aziyenda mofulumila.

Tags

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Close