National
๐๐ฅ๐ข๐ฆ๐ข ๐๐๐ณ๐๐ค๐ ๐๐ ๐๐ค๐ฎ๐ฒ๐๐ฆ๐๐๐ค๐๐ณ๐๐ซ๐ ๐๐ก๐ข๐ง๐๐ฎ ๐๐๐ฅ๐ข๐ค๐ฎ๐ฅ๐ฎ ๐ง๐๐ข ๐๐ก๐๐ง๐๐ข๐ณ๐จ ๐ฅ๐ ๐๐๐๐ ๐ค๐ฎ ๐๐ก๐ข๐ซ๐๐๐ณ๐ฎ๐ฅ๐ฎ

Wolemba Andrew Tembo
Chancy Chitsa wa zaka 19 ochokera m’mudzi mwa Mchochera, mfumu yayikulu Mpama m’boma la Chiradzulu, membala wa Matangadza Irrigation Scheme yomwe ili ndi alimi 52 watukuka ndi ngongole ya ulimi wamthilira yochokera ku National Economic Empowerment Fund (NEEF) Limited.
Mlimi wachinyamatayu ndi m’modzi mwa alimi ochuluka omwe akupindula ndi ngongole ya zipangizo za ulimi wa mthilira yomwe bungwe la NEEF likupeleka ndi cholinga chobweretsa chakudya komanso kulimbikitsa achinyamata m’Malawi muno

.
“Ndinawona NEEF ngati mwayi wodzitukula, ndichifukwa chake ndinaganiza zolima anyezi pa munda wa ekala imodzi, chifukwa ndimadziwa kuti ndi mbewu yomwe imasowa pamsika ndipo ndipanga ndalama zambiri,โ anatero Chitsa.
M’mawu ake, mkulu oyang’anira za kagawidwe kangongole ku NEEF,ย bambo Whyghtone Mweta, anayamikira chidwi cha Chitsa.
“Ndili wokondwa kuti mnyamata wamng’ono ngati uyu akuchita ulimi wotere ndipo akuganiza zodzitukula ndi masomphenya a NEEF,” adatero a Mweta,ย paulendo wowunikira m’mene ulimi wa mthilira ukuyendera ku mwera kwa Malawi.
Ngongole yi,ย ikupereka zipangizo za ulimi wamthilira monga fetereza, mbewu ndi mapampu oyendera mphamvu ya dzuwa kwa alimi kuti apeze phindu lochuluka.
Chiyambireni pologalamu ya ulimi wa mthilira chaka chino pa 14 April, 2025, bungweli lapereke ngongole zoposera MK26 biliyoni kwa alimi 64,243 m’dziko lino.
Pulogalamuyi ikuthandizira pang’onopang’ono ntchito za dziko zomwe cholinga chake ndi kuchulukitsa chakudya mdziko muno.



